Jeremiah 10

Mulungu ndi Mafano

1Inu Aisraeli, imvani zimene Yehova akunena. 2Yehova akuti,

“Musatsatire makhalidwe a anthu a mitundu ina
kapena kuchita mantha ndi zizindikiro zamlengalenga,
ngakhale anthu a mitundu ina amachita nazo mantha.
3Pakuti miyambo ya mitundu inayo ndiyachabechabe.
Iwo amakadula mtengo ku nkhalango
ndipo mmisiri amawusema ndi sompho.
4Amakongoletsa chosemacho ndi siliva ndi golide;
kenaka amachikhomerera ndi misomali
kuti chisagwedezeke.
5Mafano awo ali ngati mtengo wakanjedza woopsezera mbalame mʼmunda wa minkhaka.
Mafanowo sangathe nʼkuyankhula komwe
ndipo ayenera kunyamulidwa
popeza sangathe nʼkuyenda komwe.
Musachite nawo mantha
popeza sangathe kukuchitani choyipa
ndiponso alibe mphamvu yochitira chabwino chilichonse.”

6Palibe wofanana nanu, Inu Yehova;
Inu ndinu wamkulu,
ndipo dzina lanu lili ndi mphamvu yayikulu.
7Ndani amene angaleke kukuopani,
inu Mfumu ya mitundu ya anthu?
Chimenechi ndicho chokuyenerani.
Pakati pa anthu anzeru onse komanso mafumu onse
a mitundu ya anthu,
palibe wina wofanana nanu.
8Onsewo ndi opusa ndi opanda nzeru;
malangizo awo amawatenga kuchokera kwa mafano achabechabe opanga ndi mitengo.
9Siliva wosula amabwera naye kuchokera ku Tarisisi
ndipo golide amachokera naye ku Ufazi.
Mafanowo ndi ntchito ya anthu aluso ndi odziwa kuzokota golide.
Tsono mafanowo amawaveka zovala za mtundu wamtambo ndi pepo.
Yonseyo ndi ntchito ya anthu a luso.
10Koma Yehova ndiye Mulungu woona;
Iyeyo ndiye Mulungu wamoyo, Mfumu yamuyaya.
Akakwiya, dziko limagwedezeka;
anthu a mitundu ina sangathe kupirira ukali wakewo.
11“Awuze anthu awa kuti, ‘Milungu iyi, imene sinalenge dziko lakumwamba ndi dziko lapansi, idzawonongeka pa dziko lapansi ndi pansi pa thambo.’ ”

12Koma Mulungu analenga dziko lapansi ndi mphamvu zake;
Iye anapanga dziko lonse ndi nzeru zake
ndipo anayala thambo mwaluso lake.
13Iye akayankhula, kumamveka mkokomo wamadzi akumwamba;
Iyeyo amabweretsa mitambo kuchokera ku malekezero a dziko lapansi.
Amabweretsa mphenzi pamodzi ndi mvula
ndi kutulutsa mphepo yamkuntho kumalo kumene osungirako.

14Anthu onse ndi opusa ndiponso opanda nzeru;
mmisiri aliyense wosula golide akuchita manyazi ndi mafano ake.
Mafano akewo ndi abodza;
alibe moyo mʼkati mwawo.
15Mafanowo ndi achabechabe, zinthu zosekedwa nazo.
Pamene anthuwo azidzaweruzidwa, mafanowo adzawonongedwa.
16Koma Yehova amene ndi Cholowa cha Yakobo sali ngati mafanowo.
Iyeyu ndi Mlengi wa zinthu zonse
kuphatikizapo Israeli, mtundu umene anawusankha kuti ukhale anthu ake.
Dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.

Chiwonongeko Chikubwera

17Sonkhanitsani katundu wanu,
inu amene mukukhala mʼlinga la ankhondo.
18Pakuti Yehova akuti,
“Tsopano Ine ndidzachotsa anthu onse
amene akukhala mʼdziko lino;
adzakhala pa mavuto
mpaka adzamvetsa.”

19Aliyense ankangoti, “Mayo ine, chifukwa cha kupweteka kwanga!
Chilonda changa nʼchachikulu!”
Koma ine ndinkaganiza kuti, “Ndithu, ili ndi vuto langa basi,
choncho ndingolipirira.”
20Tenti yanga yawonongeka,
zingwe zake zonse zaduka.
Ana anga andisiya ndipo kulibenso.
Palibenso amene adzandimangire tenti,
kapena kufunyulula nsalu yake.
21Abusa ndi opusa
ndipo sanapemphe nzeru kwa Yehova;
choncho palibe chimene anapindula
ndipo nkhosa zawo zonse zabalalika.
22Tamvani! kukubwera mphekesera,
phokoso lalikulu la gulu la a ankhondo likumveka kuchokera kumpoto!
Lidzasandutsa bwinja mizinda ya ku Yuda,
malo okhala nkhandwe.

Pemphero la Yeremiya

23Inu Yehova, ndikudziwa kuti moyo umene munthu ali nawo si wake;
munthuyo sangathe kuwongolera mayendedwe ake.
24Inu Yehova, langizeni, komatu mwachilungamo,
osati ndi mkwiyo wanu,
mungandiwononge kotheratu.
25Tsanulirani ukali wanu pa mitundu ya anthu amene sakudziwani,
ndiye kuti mitundu ya anthu amene satama pa dzina lanu mopemba.
Iwo aja anasakaza Yakobo;
amusakaza kotheratu
ndipo awononga dziko lake.
Copyright information for NyaCCL